Primary site of Chmwemwe Daniel

Bengo aba nthuli

Bengo ndi mkazi wake, anapha nkhuku. Ili pa moto Bengo amaganiza kuti mkazi wake akachoka iye alawe ntchafu imodzi osadziwa kuti mkazi wake akuganizanso zomwezo.

Nkozo unamupola Bengo ndipo anapita ku toilet. Pamenepo mkazi wa ke anangonyamula chinthuli chimodzi n'kupita ku bafa kumakadya. Bengo atafika kuchokera ku toilet, anapeza mkazi wake palibe ndipo anatenganso ntchafu yosala ija nkupita ku bafa kuti naye akakhwasule.

Atatsegula anapeza mkazi wake akudya chintchafu. Mwa manyazi, Bengo anangoti "ndakubweretsera ina udyenso, wakuba iwe"

BENGO NDI MKAZI WAKE

Mai Bengo: bola akanandikwatira Satanatu. Mwina akanandisamala.

Bengo: Mukanangomangidwatu chabe chifukwa malamulo a dziko lino amaletsa kukwatirana pa chibale.

Mai Bengo: Mmmmm ?

Werengani Nkhani za Bengo zinanso

Top 3 updates

For more updates click here

no Latest Update


Back Home Up