BENGO KU BARBER SHOP

Tsiku lina Bengo analowa mu Barbershop kuyamba kumetetsa. Ali mkati mometetsa kunabwera nzimayi yemwe anali ndi saloon yake momwemo. Kenako Bengo anamulankhula nzimayi uja motere:


BENGO: Zabwino aunt!
NZIMAYI: Zabwinotu!
BENGO: Kodi mumagwira ntchito momuno eti?
NZIMAYI: Eya! Saloon ya azimayiyo ndi yanga.
BENGO: Ok! Ndie bwanji tingakumane after works? Ndakufirani bad aunt!
NZIMAYI: ndinetu wokwatiwa!. Nanga amunanga?
BENGO: Aaaaah! Inu tamutayeni kape ameneyo! Mukangomunamiza kuti mwaweruka mochedwa.
NZIMAYI: Nde mungowawuzatu nokha! ndi omwewo akukumetaniwo
Bengo: ?????


Nchfukwa chake bengo ali ometa m'mbali kufikira lero.





Back Home Up