Bengo amakonda kulezera moti tsiku lililonse amafika kwawo utsiku. Kwawo kwa bengo kunali mphepete mwa mtsinje. Nthawi zonse akachedwa amapeza mkazi wake atagona ndipo amamutsekulira chitseko.
Tsiku lina bengo adafikanso mochedwa kuchokera ku mowa ndipo adati: "ndine Bengo tatsekula." koma mai Bengo adakana ponena kuti: "inu a Bengo, lero ndie mugona panja basi. Chisakhale chiphinjo choti tsiku lililonse mukalezera ine ndikhale wokutsegulirani....."
Mai Bengo adayankhula zambiri ndipo Bengo adaziwiratu kuti mkazi wakeyo satsegula chitseko. Kenako adaganiza plan yoti alowere. Iye anatenga mwala waukulu n`kuuponyera mu mtsinje muja. Mkazi wake adatsegula chitseko kuti aone ngati Bengo ndi yemwe waziponyeradi m`madzimo.
Atangotsegula chitseko nkutuluka, Bengo adalowa mofulumira mnyumbamo nkutseka chitseko.
Mai Bengo anadandaula ataona kuti amunawo awaputsitsa ndipo adati: "nditsegulireni chonde" Bengo anati: "lero ugona panja iwe."
Werengani