Bengo mu Ndege

Bengo anali mugulu la amisala omwe amachosedwa ku Zomba mental ndipo amapita nawo ku Mzuzu kuzera pa ndege. Bengo anapita kutsogolo komwe kunali oyendetsa ndege (pilot) ndikukamuuza kuti amuphunzitse kuyendesa ndegeyo. Oyendesa ndege uja anayesesa kukana koma Bengo sanasiye kukakamila. Oyendetsa ndage uja pokumva amisala ambiri akupanga phokoso mu ndege muja [ndiponso podziwa kuti palibe angakwanise kuwaletsa kupanga phokoso,] anamuuza Bengo nati: "Ukakwanitsa kuwaletsa anzakowa kupanga phokoso, ndikuphunzitsa kuyendesa ndege." Bengo anapita komwe kunali anzake kuja. Patapita kanthawi mu ndege yonse munangoti zii popanda ngakhale m'modzi oyankhula. Kenaka Bengo anapitaso kwa oyendetsa ndege uja ndikukamuuza kuti amuphunzitse kuyendetsa. Oyendetsa ndege uja anadabwa ndipo anamufunsa Bengo nati:

  • "Iwe wakwanitsa bwanji kuwauza anzako aja kuti akhale phee chonchi?
  • Bengo: Ndinawauza koma samamvera ndiye ndinangowatsekulira chitseko kuti akatsewere paja.
  • Oyendesa ndege: ??????
  • Werengani Nkhani za Bengo zinanso




    Back Home Up