“Ndi kuno komwe network ikupedzeka”
Bengo anafika ku mudzi wina komwe anapeza kuti network ikugwira bwino. Kenako anatumiza SMS kwa mkazi wake yemwe anamsiya ku town. Mwatsoka analakwitsa nambala ndipo sms ija inapita kwa mkazi yemwe mwamuna wake anali atamwalira masiku atatu apitawo.
Namfedwayu atalandira SMS ijaanayamba kuwerenga, atamaliza pompo pompo anakomoka. Mwana wake atawona izi anatenga foni ndikuyamba kuwerenga SMS ija: "mkazi wanga wokondedwa, ndikudziwa kuti ukhala odabwa koma ndi kuno komwe network ikugwira ngati kumeneko. Ndinafika bwino moti zonse zokonzekera kuti nawe ubwere kuno zatha moti khala okonzeka chifukwa nthawi iliyonse ndibwera kudzakutenga."
Mwana naye kukomoka kunali komweko!
Werengani